Isaiah 9
1 Koma mdimawo sudzakhala mpaka kalekale! Kalekale Mulungu anachititsa manyazi maiko a Zebuloni ndi Nafutali. Koma m'tsogolo mudzakhala ulemerero! Njira ya kunyanja, tsidya lina la Yorodani, Galileya kumene kumakhala mitundu ina, kudzawala kwambiri!