Genesis 1
1 Pachiyambi Mulungu analenga zonse, nthaka yapansi, ndi thambo lamwamba.
6 Mulungu analankhulanso. "Pakhale mlengalenga kulekanitsa madzi pakati."
9 Mulungu analankhulanso. "Madzi asonkhane pamodzi. Pamtunda paoneke." Zinakhaladi choncho.
11 Mulungu analankhulanso. "Zomera zimere pa dziko lapansi. Udzu. Mitengo yobala zipatso zokhala ndi mbewu mkati mwawo." Zinakhaladi choncho.
14 Mulungu analankhulanso. "Pakhale zounikira mlengalenga kulekanitsa usana ndi usiku, kudziwitsa nyengo ndi masiku ndi zaka."