Isaiah 6
1 Mfumu Uziya anamwalira. Ndinaona Ambuye! Anakhala pampando wachifumu wautali kwambiri wofika kumwamba! Mwinjiro wake unadzaza kachisi yense!
2 Awo oyaka moto anaimirira pamwamba pake! Aliyense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi! Mapiko awiri anaphimba nkhope zawo! Mapiko awiri anaphimba mapazi awo! Mapiko awiri anawawulutsa!
5 Ndinafuula nati, "Ndatha! Ndatha! Pakamwa panga ndi padothi ndipo ndimakhala ndi anthu omwe pakamwa pawo ndi padothi! Ndipo maso anga angopenya Mfumu, Yahweh wa Magulu Ankhondo!"