Deuteronomy 32

4 Iye ndiye Thanthwe. Chilichonse chimene amachita nchangwiro. Njira iliyonse yomwe amayendamo ndi yolungama. Amasunga lonjezo lake. Sanama konse. Ndiye wabwino ndi wolungama.

8 Pamene Wam'mwambamwamba anagawa dziko, pamene anamwaza anthu pa dziko lapansi, anajambula malire a mtundu uliwonse. Anawagawanitsa malinga ndi chiwerengero cha ana a Mulungu.

15 Koma Yeshuruni anadzidyetsa n'kuyamba kuponya miyendo ngati ng'ombe yamchire. Munanenepa. Munathupika. Munakhala aulesi. Ndiyeno munataya Mulungu amene anakupangani. Munalavulira pa Thanthwe lomwe linakupulumutsani.