Deuteronomy 1
1 Mose analankhula mawu awa kwa Aisiraeli onse. Anali ataima kum'mawa kwa mtsinje wa Yorodano m'chipululu, m'dziko louma lotentha ndiponso lathyathyathya. Anamanga misasa yawo moyang'anana ndi Sufu, pakati pa Parani, Tofeli, Labani, Hazeroti, ndi Dizahabu.
19 Kenako tinachoka ku Horebu. Tinayenda m'chipululu chachikulu chochititsa mantha, munachiona ndi maso anu! Tinapita ku mapiri a Aamori, monga momwe Yahwe Mulungu wathu anatiuza. Tinafika ku Kadesi Baranea.
22 Koma nonsenu munabwera kwa ine. Munati, "Titumize amuna atitsogolere poyamba. Akayang'ane dzikolo. Kenako abwere kudzatiwuza njira yoti tidutsemo ndi mizinda imene tikaipeze."