Isaiah 61

1 Mzimu wa Ambuye Yahweh uli pa ine. Yahweh wandisankha ndi kundiyika pambali. Wandituma kudzabweretsa uthenga wabwino kwa osauka. Wandituma kudzachiritsa osweka mitima. Wandituma kudzakhazikitsa ufulu kwa ogwidwa ukapolo, ndi kuuza akaidi kuti angatuluke mu mdima.

10 Ndili wodzaza ndi chimwemwe chifukwa cha Yahweh! Moyo wanga wonse ukukondwera chifukwa cha Mulungu wanga! Wandiveka zovala za chipulumutso. Wandikulunga mkanjo wachilungamo. Ndikuoneka ngati mkwati wovala chisoti chake chachifumu, ngati mkwatibwi wokongoletsedwa ndi mikanda yake.