Genesis 2
7 Yehova Mulungu anatenga dothi pansi. Iye anaumba munthu. Anamugwerera nayamba kumupumira mpweya m'mphuno mwake. Chifuwa cha munthuyo chinatukuka. Anali moyo!
8 Yehova Mulungu anabzala munda chakum'mawa, ku Edeni. Iye anaika munthuyo kumeneko.
9 Yehova Mulungu anameresetsa mitengo pansi. Mitengo yokongola. Mitengo yodzaza ndi zipatso zabwino. Pakati pa munda panali mitengo iwiri, mtengo wa moyo komanso mtengo wodziwa chabwino ndi choipa.
16 Yehova Mulungu anamupatsa munthuyo lamulo limodzi. "Idya kuchokera ku mtengo uliwonse wa m'mundamo. Mtengo uliwonse womwe ukufuna."
18 Yehova Mulungu anati, "Sizabwino kuti munthu akhale yekha. Ndidzampangira mthandizi womuyenera."